22 Izi anacita Benaya mwana wa Yehoyada, natenga dzina mwa ngwazi zitatuzo.
23 Iye ndiye waulemu koposa makumi atatuwo, koma sadafikana ndi atatu oyamba. Ndipo Davide anamuika kuyang'anira olindirira ace.
24 Asaheli mbale wa Yoabu anali wa makumi atatuwo; Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu;
25 Sama Mharodi, Elika Mharodi;
26 Helezi Mpaliti, Ira mwana wa Ikesi Mtekoi.
27 Abiyezeri M-anetori, Mebunai Mhusati;
28 Zalimoni M-ahohi, Maharai Mnefati;