10 Toi anatumiza mwana wace Joramu kwa mfumu Davide, kuti akamlankhule iye, ndi kumdalitsa, popeza anamenyana ndi Hadadezeri ndi kumkantha; pakuti pakati pa Hadadezeri ndi Toi panali nkhondo. Ndipo Joramu anabwera ndi zotengera zasiliva, ndi zotengera zagolidi, ndi zotengera zamkuwa.