16 Koma olamulira sanadziwa uko ndinamuka, kapena cocita ine; sindidauzenso kufikira pamenepo Ayuda, kapena ansembe, kapena aufuru, kapena olamulira, kapena otsala akucita nchitoyi.
17 Pamenepo ndinanena nao, Muona coipa m'mene tirimo, kuti Yerusalemu ali bwinja, ndi zipata zace zotentha ndi moto; tiyeni, timange linga la Yerusalemu, tisakhalenso cotonzedwa.
18 Ndinawauzanso za dzanja la Mulungu wanga londikhalira mokoma, ndiponso za mau anandiuza mfumu. Nati iwo, Tinyamuke, timange. Cotero anandilimbitsira manja mokoma.
19 Koma Sanibalati Mhoroni, ndi Tobiya kapolo M-amoniyo, ndi Gesemu M-arabu, anamva natiseka pwepwete, natipeputsa, nati, Ciani ici mucicita? Mulikupandukira mfumu kodi?
20 Koma ndinawabwezera mau, ndi kunena nao, Mulungu Wam'mwamba, Iye ndiye adzatilemeza; cifukwa cace ife akapolo ace tidzanyamuka ndi kumanga; koma inu mulibe gawo, kapena ulamuliro, kapena cikumbukilo, m'Yerusalemu.