64 Awa anafunafuna maina ao m'buku la iwo owerengedwa mwa cibadwidwe, koma osawapeza; potero anawayesa odetsedwa, nawacotsa ku nchito ya nsembe.
65 Ndipo kazembe anawauza kuti asadyeko zopatulikitsa, mpaka wauka wansembe wokhala ndi Urimu ndi Tumimu.
66 Msonkhano wonse pamodzi ndiwo zikwi makumi anai ndi ziwiri mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi,
67 osawerenga akapolo ao amuna ndi akazi, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana atatu ndi makumi atatu kudza asanu ndi awiri; ndipo anakhala nao amuna ndi akazi oyimbira mazana awiri mphambu makumi anai kudza asanu ndi mmodzi.
68 Akavalo ao ndiwo mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu kudza asanu ndi mmodzi; nyuru zao mazana awiri mphambu makumi anai kudza zisanu
69 ngamira zao mazana anai mphambu makumi atatu kudza asanu aburu ao zikwi zisanu ndi cimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi awiri.
70 Ndipo ena a akuru a nyumba za makolo anapereka kunchito. Kazembeyo anapereka kucuma madariki agolidi cikwi cimodzi, mbale zawazira makumi asanu, maraya a ansembe makumi atatu.