12 Pakuti sitilimba mtima kudziwerenga, kapena kudzilinganiza tokha ndi ena a iwo amene adzibvomeretsa okha; koma iwowa, podziyesera okha ndi iwo okha, ndi kudzilinganiza okha ndi iwookha, alibe nzeru.
13 Koma ife sitidzadzitamandira popitirira muyeso, koma monga mwa muyeso wa cilekelezero cimene Mulungu anatigawira muyeso, kufikira ngakhale kwa inunso.
14 Pakuti sitinyanyampiradi tokha, monga ngati sitinafikira kwa inu; pakuti tinadza kufikira inunso, mu Uthenga Wabwino wa Kristu:
15 osadzitamandira popitirira muyeso mwa macititso a ena; koma tiri naco ciyembekezo kuti pakukula cikhulupiriro canu, tidzakulitsidwa mwa inu monga mwa cilekezero cathu kwa kucurukira,
16 kukalalikira Uthenga Wabwino m'tsogolo mwace mwa inu, sikudzitamandira mwa cilekezero ca wina, ndi zinthu zokonzeka kale.
17 Koma iye wodzitamandira adzitamandire mwa Ambuye;
18 pakuti si iye amene adzitama yekha, koma iye amene Ambuye amtama ali wobvomerezeka.