1 Cifukwa cace ndinena, Mulungu anataya anthu ace kodi? Msatero ai. Pakuti inenso ndiri M-israyeli, wa mbeu ya Abrahamu, wa pfuko la Benjamini.
2 Mulungu sanataya anthu ace amene iye anawadziwiratu, Kapena simudziwa kodi cimene lembo linena za Eliya? kuti anaumirira Mulungu poneneza Israyeli, kuti,
3 Ambuye, anawapha aneneri anu, nagwetsa maguwa anu a nsembe; ndipo ine ndatsala ndekha, ndipo alikufuna moyo wanga.
4 Koma kuyankha kwa Mulungu kudatani kwa iye? Ndinadzisiyira ndekha anthu amunazikwi zisanu ndi ziwiri, amene sanagwadira Baala.
5 Coteronso nthawi yatsopano ciripo cotsalira monga mwa kusankha kwa cisomo.
6 Koma ngati kuli ndi cisomo, sikulinso ndinchito ai; ndipo pakapanda kutero, cisomo sicikhalanso cisomo.