13 Koma ndilankhula ndi inu anthu amitundu. Popeza ine ndiri mtumwi wa anthu amitundu, millemekeza utumiki wanga;
14 kuti ngati nkutheka ndikacititse nsanje amenewo a mtundu wanga; ndi kupulumutsa ena a iwo.
15 Pakuti ngati kuwataya kwao kuli kuvanianitsa kwa dziko lapansi, nanga kulandiridwa kwao kudzatani, koma ndithu ngati moyo wakucokera kwa: akufa?
16 Ndipo ngati zoundukula ziri zopatulika, coteronso mtanda; ndipo ngati muzu uli wopatulika, coteronso nthambi.
17 Koma ngati nthambi zina zinathyoledwa, ndipo iwe, ndiwe mtengo wazitona wa kuthengo, unamezetsanidwa mwa izo, nugawana nazo za muzu za mafuta ace a mtengowo,
18 usadzitama iwe wekha pa nthambizo: koma ngati udzitama wekha, suli iwe amene unyamula muzu, ai, koma muzu ukunyamula iwetu.
19 Ndipo kapena udzanena, Nthambizo zathyoledwa kuti ine ndikamezetsanidwe nao.