27 Ndipo ici ndi cipangano canga ndi iwo,Pamene ndidzacotsa macimo ao.
28 Kunena za Uthenga Wabwino, iwo ali ngati adani, cifukwa ca inu; koma kunena za cisankhidwe, z ali okondedwa, cifukwa ca makolo.
29 Pakuti 1 mphatso zace ndi kuitana kwace kwa Mulungu sizilapika.
30 Pakuti 2 monga inunso kale simunamvera Mulungu, koma tsopano mwalandira cifundo mwa kusamvera kwao,
31 coteronso iwo sanamvera tsopano, kuti iwonso akalandire cifundo, cifukwa ca cifundo ca kwa inu.
32 Pakuti 3 Mulungu anatsekera pamodzi onse m'kusamvera, kuti akacitire onse cifundo.
33 Ha! kuya kwace kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwace kwa Mulungu! 4 Osasanthulikadi maweruzo ace, ndi njira zace nzosalondoleka!