3 Ambuye, anawapha aneneri anu, nagwetsa maguwa anu a nsembe; ndipo ine ndatsala ndekha, ndipo alikufuna moyo wanga.
4 Koma kuyankha kwa Mulungu kudatani kwa iye? Ndinadzisiyira ndekha anthu amunazikwi zisanu ndi ziwiri, amene sanagwadira Baala.
5 Coteronso nthawi yatsopano ciripo cotsalira monga mwa kusankha kwa cisomo.
6 Koma ngati kuli ndi cisomo, sikulinso ndinchito ai; ndipo pakapanda kutero, cisomo sicikhalanso cisomo.
7 Ndipo ciani tsono? ici cimene Israyeli afunafuna sanacipeza; koma osankhidwawo anacipeza, ndipo otsalawo anaumitsidwa mtima;
8 monga kunalembedwa kuti, Mulungu anawapatsa mzimu watulo, maso kuti asapenye, ndi makutu kuti asamve, kufikira lero lino.
9 Ndipo Davide akuti,Gome lao likhale kwa iwo, ngati msampha, ndi ngati diwa,Ndi monga cokhumudwitsa, ndi cowabwezera cilango;