1 Anthu onse amvere maulamuliro a akulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wocokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu.
2 Kotero kuti iye amene atsutsana nao ulamuliro, akaniza coikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza, adzadzitengera kulanga
3 Pakuti mafumu sakhala oopss nchito zabwino koma zoipa. Ndipo ufuna kodi kusaopa ulamuliro: Cita cabwino, ndipo udzalandirs kutama m'menemo:
4 pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kucitira iwe zabwino. Koma ngati ucita coipa opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwacabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwe zera cilango wocita zoipa.
5 Cifukwa cace, kuyenera kuti mukhale omvera, si cifukwa ca mkwiyo woo kha, komanso cifukwa ca cikumbu mtima.
6 Pakuti cifukwa ca ici mupatsanso msonkho; pakuti iwo ndi wo atumiki a Mulungu akulabadira be cinthu cimeneci.
7 Perekani kwa anthu onse mangawa ao; msonkho kwa eni ace a msonkho; kuli pira kwa eni ace a kulipidwa; kuopa kwa eni ace a kuwaopa; ulemu kwe eni ace a ulemu.