5 Cifukwa cace, kuyenera kuti mukhale omvera, si cifukwa ca mkwiyo woo kha, komanso cifukwa ca cikumbu mtima.
6 Pakuti cifukwa ca ici mupatsanso msonkho; pakuti iwo ndi wo atumiki a Mulungu akulabadira be cinthu cimeneci.
7 Perekani kwa anthu onse mangawa ao; msonkho kwa eni ace a msonkho; kuli pira kwa eni ace a kulipidwa; kuopa kwa eni ace a kuwaopa; ulemu kwe eni ace a ulemu.
8 Musakhale ndi mangawa kwa munthu ali yense, koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mnzace wakwanitsa lamulo.
9 Pakuti ili, Usacite cigololo, Usaphe, Usabe, Usasirire, ndipo lingakhale lamulo lina liri lonse, limangika pamodzi m'mau amenewa, kuti, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe wekha.
10 Cikondano sicicitira mnzace coipa; cotero cikondanoco ciri cokwanitsa lao mulo.
11 Ndipo citani ici, podziwa inu nyengo, kuti tsopano ndiyo nthawi yabwino yakuuka kutulo; pakuti tsopano cipulumutso cathu ciri pafupi koposa pamene tinayamba kukhulupira.