15 Miyendo yao icita liwiro kukhetsa mwazi;
16 Kusakaza ndi kusauka kuli m'njira zao;
17 Ndipo njira ya mtendere sanaidziwa;
18 Kumuopa Mulungu kulibe pamaso pao.
19 Ndipo tidziwa kuti zinthu ziri zonse cizinena cilamulo cizilankhulira iwo ali naco cilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;
20 cifukwa kuti pamaso pace palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi Debito za lamulo; pakuti ucimo udziwika ndi lamulo.
21 Koma tsopano cilungamo ca Mulungu caoneka copanda lamulo, cilamulo ndi aneneri acitira ici umboni;