17 Ndipo tsopano si ine ndicicita, koma ucimo wakukhalabe m'kati mwanga ndiwo.
18 Pakuti ndidziwa kuti m'kati mwanga, ndiko m'thupi langa, simukhala cinthu cabwino; pakuti kufuna ndiri nako, koma kucita cabwino sindikupeza.
19 Pakuti cabwino cimene ndicifuna, sindicicita; koma coipa cimene sindicifuna, cimeneco ndicicita.
20 Koma ngati ndicita cimene sindicifuna, si ndinenso amene ndicicita, koma ucimo wakukhalabe m'kati mwanga ndiwo.
21 Ndipo cotero odipeza lamulo ili, kuti, pamene ndifuna cabwino, coipa ciriko.
22 Pakuti monga mwa munthu wa m'kati mwanga, ine ndikondwera ndi cilamulo ca Mulungu:
23 koma ndiona lamulo lina m'ziwalo zanga, lirikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la m'ziwalo zanga.