3 Ndipo cifukwa cace, ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina, pokhala mwamuna wace wamoyo, adzanenedwa mkazi wacigololo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamuloli; cotero sakhala wacigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.
4 Cotero, abale anga, inunso munayesedwa akufa ku cilamulo ndi thupi la Kristu; kuti mukakhale ace a wina, ndiye amene anaukitsidwa kwa akufa, kuti ife timbalire Mulungu zipatso,
5 Pakuti pamene tinali m'thupi, zilakolako za macimo, zimene zinali mwa cilamulo, zinalikucita m'ziwalo zathu, kuti zibalire imfa zipatso,
6 Koma tsopano tinamasulidwa kucilamulo, popeza tinafa kwa ici cimene tinagwidwa naco kale; cotero kuti titumikire mu mzimu watsopano, si m'cilembo cakale ai.
7 Pamenepo tidzatani? Kodi cilamulo ciri ucimo? Msatero ai. Koma ine sindikadazindikira ucimo, koma mwa lamulo ndimo; pakuti sindikadazindikira cilakolako sicikadati cilamulo, Usasirire;
8 koma ucimo, pamene unapeza cifukwa, unacita m'kati mwanga zilakolako zonse mwa lamulo; pakuti popanda lamulo ucimo uli wakufa.
9 Ndipo kale ine ndinali wamoyo popanda lamulo; koma pamene lamulo linadza, ucimo unatsitsimuka, ndipo ine ndinafa.