13 pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zocita zace za thupi, mudzakhala ndi moyo.
14 Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu,
15 Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kucitanso mantha; koma munalandira mzimu waumwana, umene tipfuula nao, kuti, Abba, Atate,
16 Mzimu yekha acita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu;
17 ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ace a Mulungu, ndi olowa anzace a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalaodirenso ulemerero pamodzi ndi iye.
18 Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife.
19 Pakuti ciyembekezetso ca colengedwa cilimilia bvumbulutso la ana a Molungu.