27 ndipo iye amene asanthula m'mitima adziwa cimene acisamalira Mzimu, cifukwa apempherera oyera mtima monga mwa cifuno ca Mulungu.
28 Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwacitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wace.
29 Cifukwa kuti iwo 1 amene iye anawadziwiratu, 2 iwowa anawalamuliratu 3 afanizidwe ndi cifaniziro ca Mwana wace, kuti 4 iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri;
30 ndipo amene iye anawalamuliratu, iwo anawaitananso; ndimo iwo amene iye anawaitana, iwowa anawayesanso olungama; ndi iwo amene iye anawayesa olungama, 5 iwowa anawapatsanso olemerero.
31 Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? 6 Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?
32 iye amene sanatimana Mwana wace wa iye yekha, koma 7 anampereka cifukwa ca ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi iye?
33 Ndani adzaneneza osankhidwa a Mulungu? 8 Mulungu ndiye ameneawayesa olungama;