1 Ndipo pamene iwo anayandikira ku Yerusalemu, ku Betefage ndi Betaniya, pa phiri la Azitona, anatuma awiri a ophunzira ace,
2 nanena nao, Mukani, lowani m'mudzi wapandunji ndi inu; ndipo pomwepo pakulowamo mudzapeza mwana wa buru womangidwa, amene palibe munthu anakhalapo kale lonse; mmasuleni, ndipo mubwere naye.
3 Ndipo munthu akati kwa inu, Mutero bwanji? Katini, Ambuye amfuna iye; ndipo pomwepo adzamtumiza kuno.
4 Ndipo anacoka, napeza mwana wa buru womangidwa pakhomo, pabwalo m'khwalala, nammasula iye.
5 Ndipo ena akuima kumeneko ananena nao, Mucita ciani ndi kumasula mwana wa buru?
6 Ndipo anati kwa iwo monga momwe ananena Yesu: ndipo anawalola iwo apite naye.
7 Ndipo anabwera naye mwana wa buru kwa Yesu, naika zobvala zao pa iye, ndipo Iye anakhala pamenepo.