11 Ndipo Iye analowa m'Yerusalemu, m'Kacisi; ndipo m'mene anaunguza zinthu zonse, popeza ndi madzulo, anaturuka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwoo.
12 Ndipo m'mawa mwace, ataturuka ku Betaniya, Iye anamva njala.
13 Ndipo anaona mkuyu kutali, uli ndi masamba; ndipo anadza Iye, kuti kapena akapezapo kanthu: ndipo m'mene anafikako anapeza palibe kanthu koma masamba okha; pakuti siinali nyengo yace ya nkhuyu.
14 Ndipo anayankha nanena ndi uwo, Munthu sadzadyanso zipatso zako nthawi zonse. Ndipo ophunzira ace anamva,
15 Ndipo anafika iwo ku Yerusalemu; ndipo Iye analowa m'Kacisi, nayamba kuturutsa akugulitsa ndi akugula malonda m'Kacisimo, nagubuduza magome a osinthana ndalama, ndi mipando yaogulitsa nkhunda;
16 ndipo sanalola munthu ali yense kunyamula cotengera kupyola pakati pa Kacisi.
17 Ndipo anaphunzitsa, nanena nao, Sicilembedwa kodi, Nyumba yanga idzachedwa nyumba yakupempheramo anthu a mitundu yonse? koma inu mwaiyesa phanga la acifwamba.