1 Ndipo Iye anayamba kulankhula nao m'mafanizo. Munthu analima munda wamphesa, nauzunguniza ndi linga, nakumba moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.
2 Ndipo m'nyengo yace anatuma kapolo kwa olimawo, kuti alandireko kwa olimawo zipatso za m'munda wamphesa.
3 Ndipo iwo anamtenga iye, nampanda, namcotsa wopanda kanthu.
4 Ndipo anatumanso kapolo wina kwa iwo; ndipo ameneyu anamlasa mutu, namcitira zomcititsa manyazi.
5 Ndipo anatuma wina; iyeyu anamupha; ndi ena ambiri; ena anawapanda, ndi ena anawapha.
6 Anamtsalira mmodzi, ndiye mwana wace wokondedwa; potsiriza anamtuma iye kwa iwo, nanena, Adzamcitira ulemu mwana wanga.
7 Koma olima ajawo, ananena mwa iwo okha, Ameneyu ndiye wolowa nyumba; tiyeni timuphe iye, ndipo mundawu udzakhala wathu.