1 Ndipo popita masiku awiri kuli phwando la Paskha ndi mikate yopanda cotupitsa; ndipo ansembe akuru ndi alembi anafunafuna momcitira ciwembu, ndi kumupha:
2 pakuti anati, Paphwando ai, kuti pangakhale phokoso la anthu.
3 Ndipo pakukhala iye ku Betaniya m'nyumba ya Simoni wakhate, m'mene anaseama kudya, anadzapo mkazi ali nayo nsupa yaalabastero ya mafuta onunkhira bwino a nardo weni weni a mtengowapatali; naswa nsupayo, nawatsanulira pamutu pace.
4 Koma anakhalako ena anabvutika mtima mwa iwo okha, ndi kuti, Mafutawo atayidwa cifukwa ninji?
5 Pakuti mafuta amene akadagula marupiya atheka mazana atatu ndi mphambu zace, ndi kupatsa aumphawi. Ndipo anadandaulira mkaziyo.
6 Koma Yesu anati, Mlekeni, mumbvutiranji? wandicitira Ine nchito yabwino.