38 Ndipo cinsart cocinga ca m'Kacisi cinang'ambika pakati, kuyambira kumwamba kufikira pansi.
39 Ndipo pamene kenturiyo, woimirirapo popenyana ndi Iye, anaona kuti anapereka mzimu kotero, anati, Zoonadi, munthu uyu anali Mwana wa Mulungu.
40 Ndipo analinso kumeneko akazi akuyang'anira kutali; mwa iwo anali Maliya wa Magadala, ndi Maliya amace wa Yakobo wamng'ono ndi wa Yose, ndi Salome;
41 amene anamtsata Iye, pamene anali m'Galileya, namtumikira; ndi akazi ena ambiri, amene anakwera kudza ndi Iye ku Yerusalemu.
42 Ndipo atafika tsono madzulo, popeza mpa tsiku lokonzera, ndilo la pambuyo pa Sabata,
43 anadzapo Y osefe wa ku Arimateya, mkulu wa mirandu womveka, amene yekha analikuyembekezera Ufumu wa Mulungu; nalimba mtima nalowa kwa Pilato, napempha mtembo wace wa Yesu.
44 Ndipo Pilato anazizwa ngati adamwaliradi; naitana kenturiyo, namfunsa ngati adamwalira kale.