8 Ndipo khamu la anthu anabwera nayamba kupempha kuti acite monga adafuwacitira.
9 Ndipo Pilato anawayankha, nanena nao, Kodi mufuna kuti ndikumasulireni Mfumu ya Ayuda?
10 Pakuti anazindikira kuti ansembe akuru anampereka Iye mwanjiru.
11 Koma ansembe akuru anasonkezera khamulo, kuti makamaka awamasulire Baraba.
12 Ndipo Pilato anawayankhanso, nati kwa iwo, Pamenepo ndidzacita ciani ndi Iye amene mumchula Mfumu ya Ayuda?
13 Ndipo anapfuulanso, Mpacikeni pamtanda.
14 Ndipo Pilato ananena nao, Pakuti Iye anacita coipa cotani? Koma iwo anapfuulitsatu, Mpacikeni Iye.