1 Ndipo litapita Sabata, Maliya wa Magadala, ndi Maliya amace wa Yakobo, ndi Salome, anagula zonunkhira, kuti akadze kumdzoza Iye.
2 Ndipo anadza kumanda mamawa tsiku loyamba la Sabata, litaturuka dzuwa.
3 Ndipo analikunena mwa okha, Adzatikunkhunizira ndam mwalawo, pa khomo la manda?
4 Ndipo pamene anakweza maso anaona kuti mwala wakunkhunizidwa pakuti unali waukuru ndithu.
5 Ndipo pamene analowa m'manda, anaona mnyamata alikukhala ku mba li va ku dzanja lamanja, wobvala mwinjiro woyera; ndipo iwo anadabwa.
6 Ndipo iye ananena nao, Musadabwe: mulikufuna Yesu Mnazarene amene anapacikidwa: anauka; sali pano; taonani, mbuto m'men e anaikamo Iye!
7 Koma mukani, uzani ophunzira ace, ndi Petro, kuti akutsogolerani inu ku Galileya; kumeneko mudzamuona Iye, monga ananena ndi inu.