3 Ndipo anadza kwa Iye otenga munthu wodwala manjenje, wonyamulidwa ndi anthu anai.
4 Ndipo pamene sanakhoza kufika kuli Iye, cifukwa ca khamu la anthu, anasasula chindwi pokhala Iye; ndipo pamene anatha kuliboola, anatsitsa mphasa m'mene alinkugonamo wodwala manjenjeyo,
5 Ndipo Yesu pakuona cikhulupiriro cao ananena ndi wodwala manjenje, Mwana, macimo ako akhululukidwa.
6 Koma anakhalapo ena a alembi akuganizira mumtima mwao,
7 Munthu amene atero bwanji? acita mwano; akhoza ndani kukhululukira macimo, koma mmodzi, ndiye Mulungu?
8 Ndipo pomwepo Yesu pozindikira mumtima mwace kuti alikuganizira comweco mwa iwo okha, ananena nao, Muganiza bwanji zinthu izi m'mitima yanu?
9 Capafupi nciti, kapena kuuza wodwala manjenje kuti, Macimo ako akhululukidwa; kapena kuti, Nyamuka, senza mphasa yako, nuyende?