24 Ndipo ananena nao, Yang'anirani cimene mukumva; ndi muyeso umene muyesera nao udzayesedwa kwa inu; ndipo kudzaonjezedwa kwa inu.
25 Pakuti kwa iye amene ali nako kanthu, kadzapatsidwa; ndipo kwa iye amene alibe kanthu, kadzacotsedwa ngakhale kanthu kali konse ali nako.
26 Ndipo ananena, Ufumu wa Mulungu uli wotero, monga ngati munthu akataya mbeu panthaka;
27 nakagona ndi kuuka, usiku ndi usana, ndipo mbeu zikamera, ndi kukula, iye sadziwa umo zicitira.
28 Nthaka ibala zipatso zace yokha; uyamba mmera, zitsata ngala, pamenepo maso okhwima m'ngalamo.
29 Pakucha zipatso, pamenepo atumiza zenga, pakuti nthawi yakumweta yafika.
30 Ndipo ananena, Tidzafaniziranji Ufumu wa Mulungu? kapena tidzaulinganiza ndi fanizo lotani?