25 Pakuti kwa iye amene ali nako kanthu, kadzapatsidwa; ndipo kwa iye amene alibe kanthu, kadzacotsedwa ngakhale kanthu kali konse ali nako.
26 Ndipo ananena, Ufumu wa Mulungu uli wotero, monga ngati munthu akataya mbeu panthaka;
27 nakagona ndi kuuka, usiku ndi usana, ndipo mbeu zikamera, ndi kukula, iye sadziwa umo zicitira.
28 Nthaka ibala zipatso zace yokha; uyamba mmera, zitsata ngala, pamenepo maso okhwima m'ngalamo.
29 Pakucha zipatso, pamenepo atumiza zenga, pakuti nthawi yakumweta yafika.
30 Ndipo ananena, Tidzafaniziranji Ufumu wa Mulungu? kapena tidzaulinganiza ndi fanizo lotani?
31 Ngati mbeu yampiru, imene ikafesedwapanthaka, ingakhale icepa ndi mbeu zonse za padziko,