2 Ndipo pofika dzuwa la Sabata, anayamba kuphunzitsa m'sunagoge; ndipo ambiri anamva Iye, nazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti izi? Nzeru yopatsidwa kwa munthuyu njotani, ndi zamphamvu zotere zocitidwa ndi manja ace?
3 Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Mariya, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yuda, ndi Simoni? Ndipo alongo ace sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye.
4 Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu, koma m'dziko la kwao ndimo, ndi pakati pa abale ace, ndi m'nyumba yace.
5 Ndipo kumeneko sanakhoza Iye kucita zamphamvu konse, koma kuti anaika manja ace pa anthu odwala owerengeka, nawaciritsa.
6 Ndipo anazizwa cifukwa ca kusakhulupirira kwao. Ndipo anayendayenda m'midzi yozungulirapo, naphunzitsa.
7 Ndipo anadziitanira khumi ndi awiriwo, nayamba kuwatumiza Iwo awiri awiri; nawapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa;
8 ndipo anawauza kuti asatenge kanthu ka paulendo, koma ndodo yokha; asatenge mkate, kapena thumba, kapena ndalama m'lamba lao;