9 koma abvale nsapato; ndipo anati, Musabvale malaya awiri.
10 Ndipo ananena nao, Kumene kuli konse mukalowa m'nyumba, khalani komweko kufikira mukacokako.
11 Ndipo pamalo ponse sakulandirani, kapena kumvera inu, pakucoka kumeneko, sansani pfumbi liri ku mapazi anu, likhale mboni ya kwa iwo.
12 Ndipo anaturuka nalalikira kuti anthu atembenuke mitima.
13 Ndipo anaturutsa mizimu yoipa yambiri, nadzoza mafuta anthu ambiri akudwala, nawaciritsa.
14 Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lace lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo cifukwa cace mphamvu izi zicitacita mwa Iye.
15 Koma ena ananena, kuti, Ndiye Eliya, Anati enanso, Ndiye mneneri, monga ngati mmodzi wa aneneriwo,