2 Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nakwera nao pa phiri lalitali padera pa okha; ndipo anasandulika pamaso pao:
3 ndipo zobvala zace zinakhala zonyezimira, zoyera mbu; monga ngati muomba wotsuka nsaru pa dziko lapansi sangathe kuziyeretsai.
4 Ndipo anaonekera kwa iwo Eliya ndi Mose, alikulankhulana ndi Yesu.
5 Ndipo Petro anayankha, nanena ndi Yesu, Rabi, kutikomera ife kukhala pano; ndipo timange misasa itatu; umodzi wa inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya.
6 Pakuti sanadziwa cimene adzayankha; cifukwa anacita mantha ndithu.
7 Ndipo panadza mtambo wakuwaphimba iwo; ndipo mau munaturuka m'mtambomo, kuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa; mverani Iye.
8 Ndipo dzidzidzi pounguzaunguza, sanapenya munthu wina yense, koma Yesu yekha, ndi iwo eni.