5 Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuza, Udziwa bwang kuti Sauli ndi Jonatani mwana wace anafa?
6 Mnyamata wakumuuzayo nati, Pamene ndinangoyenda pa phiri la Giliboa, ndinaona, Sauli alikuyedzamira nthungo yace, ndi magareta ndi apakavalo anamyandikiza.
7 Ndipo iye pakuceukira m'mbuyo mwace anandiona, nanditana. Ndipo ndinayankha, Ndine.
8 Nanena, Ndiwe yani? Ndipo ndinayankha kuti, Ndine M-amaleki.
9 Ndipo anati kwa ine, Uime pa ine nundiphe, cifukwa kuwawa mtima kwandigwera ine, popeza ndikali moyobe.
10 M'mwemo ndinakhala pambali pace ndi kumtsiriza cifukwa ndinadziwa kuti sangakhalenso ndi moyo wace, atagwa. Ndipo ndinatenga korona wa pamutu pace, ndi cigwinjiri ca pa mkono wace, ndabwera nazo kuno kwa mbuye wanga.
11 Pomwepo Davide anagwira zobvala zace nazing'amba; nateronso anthu onse okhala naye.