4 Ndipo pamene mkazi wa ku Tekowayo anati alankhule ndi mfumuyo, anagwa nkhope yace pansi namlambira, nati, Ndithandizeni mfumu.
5 Ndipo mfumuyo inanena naye, Usowanji? iye nayankha, Zoonadi ine ndine mkazi wamasiye, mwamuna wanga ana mwalira.
6 Ndipo mdzakazi wanu ndinali nao ana amuna awiri, ndipo awiriwa analimbana kumunda, panaboo wina wakuwaletsa, koma wina anakantha mnzace namupha.
7 Ndipo onani, cibale conse cinaukira mdzakazi wanu, ndi kuti, Upereke iye amene anakantha mbale wace, kuti timuphe cifukwa ca moyo wa mbale wace amene anamupha; koma pakutero adzaononga wolowa yemwe; comweco adzazima khara langa lotsala, ndipo sadzasiyira mwamuna wanga dzina kapena mbeu kunja kuno.
8 Ndipo mfumu inanena ndi mkaziyo, Pita ku nyumba yako, ndipo ndidzalamulira za iwe.
9 Ndipo mkazi wa ku Tekowayo ananena ndi mfumu, Mbuye wanga mfumu, mphulupulu ikhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga; ndipo mfumu ndi mpando wacifumu wao zikhale zopanda cifukwa.
10 Ndipo mfumu inati, Ubwere naye kwa ine ali yense wakunena kanthu ndi iwe, ndipo iyeyo sadzakukhudzanso.