1 Ndipo Davide analankhula kwa Yehova mau a nyimbo iyi tsikuli Yehova anampulumutsa m'dzanja la adani ace onse, ndi m'dzanja la Sauli.
2 Ndipo anati:-Yehova ndiye thanthwe langa, ndi ngaka yanga, ndi mpulumutsi wanga, wangadi;
3 Mulungu wa thanthwe langa, Iye ndidzamkhulupirira;Cikopa canga, ndi nyanga ya cipulumutso canga, nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga;Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuciwawa.
4 Ndidzaitanakwa Yehovaamene ayenera timtamande;Comweco ndidzapulumutsidwa kwa adani anga.
5 Pakuti mafunde a imfa anandizinga,Mitsinje ya zopanda pace inandiopsa ine.
6 Zingwe za kumanda zinandizingira;Misampha ya imfa inandifikira ine.