11 Ndipo iye anaberekeka pa Kerubi nauluka;Inde anaoneka pa mapiko a mphepo,
12 Ndipo anayesa mdimawo ngati mahema omzungulira iye,Kusonkhana kwa madzi ndi mitambo yocindikira ya mlengalenga.
13 Ceza ca pamaso paceMakala a mota anayaka,
14 Yehova anagunda kumwamba;Ndipo Wam'mwambamwamba ananena mau ace.
15 Ndipo iye anatumiza mibvi, nawawaza;Mphezi, nawaopsa,
16 Pamenepo m'munsi mwa nyanja munaoneka,Maziko a dziko anaonekera poyera,Ndi mthonzo wa Yehova,Ndi mpumo wa mweya wa m'mphuno mwace.
17 Iye anatumiza kucokera kumwamba nanditenga;Iye ananditurutsa m'madzi akuru;