15 Ndipo iye anatumiza mibvi, nawawaza;Mphezi, nawaopsa,
16 Pamenepo m'munsi mwa nyanja munaoneka,Maziko a dziko anaonekera poyera,Ndi mthonzo wa Yehova,Ndi mpumo wa mweya wa m'mphuno mwace.
17 Iye anatumiza kucokera kumwamba nanditenga;Iye ananditurutsa m'madzi akuru;
18 Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,Kwa iwo akudana ndi ine; pakuti anandiposa mphamvu,
19 Anandifikira ine tsiku la tsoka langa;Koma Yehova anali mcirikizo wanga,
20 Iye ananditurutsanso ku malo akuru;Iye anandipulumutsa, cifukwa akondwera ndi ine.
21 Yehova anandibwezera monga mwa colungama canga;Monga mwa kuvera kwa manja anga anandipatsa mphotho.