22 Pakuti ndinasunga njira za Yehova,Osapambukira koipa kusiya Mulungu wanga.
23 Pakuti maweruzo ace onse anali pamaso panga;Ndipo za malemba ace, sindinawapambukira.
24 Ndinakhalanso wangwiro kwa iye,Ndipo ndinadzisunga kusacita kuipa kwanga.
25 Cifukwa cace Yehova anandibwezera monga mwa colungama canga;Monga mwa kuyera kwanga pamaso pace.
26 Ndi acifundo Inu mudzadzionetsa wacifundo,Ndi munthu wangwiro mudzadzionetsa wangwiro;
27 Ndi oyera mtima mudzadzionetsa woyera mtima;Ndi otsutsatsutsa mudzadzionetsa wopotoza.
28 Ndipo mudzapulumutsa anthu osautsidwa;Koma maso anu ali pa odzikuza kuti muwacepetse.