1 Pambuyo pace Davide anamemezanso osankhika onse a m'Israyeli, anthu zikwi makumiatatu.
2 Ndipo Davide ananyamuka, namuka nao anthu onse anali naye, nacokera ku Baale-Yuda natengako likasa la Mulungu, limene amachula nalo Dzinalo Dzina la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa Akerubi.
3 Ndipo iwo ananyamulira likasa la Mulungu pa gareta watsopano, ataliturutsa m'nyumba ya Abinadabu, iri pacitunda, ndipo Uza ndi Ahio ana a Abinadabu anayendetsa ng'ombe za pa gareta watsopanoyo.
4 Poturuka nalo tsono pamodzi ndi likasa la Mulungu m'nyumba ya Abinadabu iri pacitunda, Ahio anatsogolera likasalo.
5 Ndipo Davide ndi a nyumba yonse ya Israyeli anasewera pamaso pa Yehova, ndi zoyimbira za mitundu mitundu za mlombwa, ndi azeze, ndi zisakasa ndi malingaka, ndi masece, ndi nsanje.