9 Pakuti ili, Usacite cigololo, Usaphe, Usabe, Usasirire, ndipo lingakhale lamulo lina liri lonse, limangika pamodzi m'mau amenewa, kuti, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe wekha.
10 Cikondano sicicitira mnzace coipa; cotero cikondanoco ciri cokwanitsa lao mulo.
11 Ndipo citani ici, podziwa inu nyengo, kuti tsopano ndiyo nthawi yabwino yakuuka kutulo; pakuti tsopano cipulumutso cathu ciri pafupi koposa pamene tinayamba kukhulupira.
12 Usiku wapita, ndi dzuwa layandikira; cifukwa cace tibvule nchito za mdima, ntibvale camuna ca kuunika.
13 Tiyendeyeode koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'cigololo ndi conyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai.
14 Koma bvalani inu Ambuye Yesu-Kristu, ndipo musaganizire za thupi kucita zofuna zace.