4 Izo ndizo mitengo iwiri ya azitona ndi zoikapo nyali ziwiri zakuima pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.
5 Ndipo wina akafuna kuipsa izo, moto uturuka m'kamwa mwao, nuononga adani ao; ndipo wina akafuna kuipsa izo, maphedwe ace ayenera kutero.
6 Izo ziti nao ulamuliro wakutseka m'mwamba, isagwe mvula masiku a cinenero cao; ndipo ulamuliro ziti nao pamadzi kuwasandutsa mwazi, ndi kupanda dziko ndi mliri uli wonse nthawi iri yonse zikafuna.
7 Ndipo pamene zidatsiriza umboni wao cirombo eokwera kuturuka m'phompho cidzacita nazo nkhondo, nicidzazilaka, nicidzazipha izo.
8 Ndipo mitembo yao idzakhala pa khwalala la mudzi waukuru, umene uchedwa, ponena zacizimu, Sodoma ndi Aigupto, pameneponso Ambuye wao anapacikidwa.
9 Ndipo a mwa anthu ndi mafuko, ndi manenedwe, ndi mitundu apenyera mitembo yao masiku atatu ndi nusu lace, osalola mitembo yao iikidwe m'manda.
10 Ndipo iwo akukhala padziko adzakondwerera, nasekerera, nadzatumizirana mitulo; popeza aneneri awa awiri anazunza iwo akukhala padziko.