8 Ndipo mitembo yao idzakhala pa khwalala la mudzi waukuru, umene uchedwa, ponena zacizimu, Sodoma ndi Aigupto, pameneponso Ambuye wao anapacikidwa.
9 Ndipo a mwa anthu ndi mafuko, ndi manenedwe, ndi mitundu apenyera mitembo yao masiku atatu ndi nusu lace, osalola mitembo yao iikidwe m'manda.
10 Ndipo iwo akukhala padziko adzakondwerera, nasekerera, nadzatumizirana mitulo; popeza aneneri awa awiri anazunza iwo akukhala padziko.
11 Ndipo atapita masiku atatu ndi nusu lace mzimu wamoyo wocokera kwa Mulungu unawalowera, ndipo anakhala ciriri; ndipomantha akuru anawagwera iwo akuwapenya.
12 Ndipo anamva mau akuru akucokera Kumwamba akunena nao, Kwerani kuno. Ndipo anakwera kumka Kumwamba mumtambo; ndipo adani ao anawapenya.
13 Ndipo panthawipo panali cibvomezi cacikuru, ndipo limodzi la magawo khumi a mudzi Iidagwa; ndipo anaphedwa m'cibvomezico anthu zikwi zisanu ndi ziwiri; ndipo otsalawo anakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa m'Mwamba.
14 Tsoka laciwiri lacoka; taonani, tsoka lacitatu lidza msanga.