17 Ndipo mngelo wina anaturuka m'Kacisi ali m'Mwamba, nakhala nalo zenga lakuthwa nayenso.
18 Ndipo mngelo wina anaturuka pa guwa la nsembe, ndiye wakukhala nao ulamuliro pamoto; napfuula ndi mau akuru kwa iye wakukhala nalo zenga lakuthwa, nanena, 1 Tumiza zenga lako lakuthwa, nudule matsango a munda wampesa wa m'dziko; pakuti mphesa zace zapsa ndithu.
19 Ndipo mngelo anaponya zenga lace ku dziko nadula mphesa za m'munda wa m'dziko, 2 naziponya moponderamo mphesa mwamukuru mwa mkwiyo wa Mulungu.
20 Ndipo 3 moponderamo mphesa anamuponda kunja kwa mudzi, ndipo mudaturuka mwazi moponderamo mphesa, kufikira zapakamwa za akavalo, kufikira mastadiya cikwi ndi mazana asanu ndi limodzi.