3 ndipo uli naco cipiriro, ndipo walola cifukwa ca dzina langa, wosalema.
4 Koma ndiri nako kanthu kotsutsana ndi iwe, kuti unataya cikondi cako coyamba.
5 Potero kumbukila kumene wagwerako, nulape, nucite nchito zoyamba; koma ngari sutero, ndidzadza kwa iwe, ndipo ndidzatunsa coikapo nyali cako, kucicotsa pamalo pace, ngati sulapa.
6 Koma ici uli naco, kuti udana nazo nchito za Anikalai, zimene Inenso ndidana nazo.
7 Iye wokhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo, K wa iye amene alakika ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli m'Paradaiso wa Mulungu.
8 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Smurna lemba;Izi anena woyamba ndi wotsiriza, amene anakhala wakufa, nakhalanso ndi moyo:
9 Ndidziwa cisautso cako, ndi umphawi wako (komatu uli wacuma), ndi mwano wa iwo akunena za iwo okha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu sunagoge wa Satana.