5 ndipo mmodzi wa akuru ananena ndi ine, Usalire: taona, Mkango wocokera m'pfuko la Yuda, Muzu wa Davide, walakika kutsegula buku ndi zizindikilo zace zisanu ndi ziwiri.
6 Ndipo ndinaona pakati pa mpando wacifumu ndi zamoyo zinai, ndi pakati pa akuru, Mwanawankhosa ali ciriri ngati waphedwa; wokhala nazo nyanga zisanu ndi ziwiri, ndi maso asanu ndi awiri, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, yotumidwa ilowe m'dziko lonse.
7 Ndipo anadza, nalitenga ku dzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wacifumu.
8 Ndipo pamene adatenga bukulo, zamoyo zinai ndi akulu makumi awiri mphambu anai zinagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse ziri nao azeze, ndi mbale zagolidi zodzala ndi zofukiza, ndizo mapemphero a oyera mtima.
9 Ndipo ayimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikilo zace; cifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,
10 ndipo mudawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo acita ufumu padziko.
11 Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva mau a angelo ambiri pozinga mpando wacifumu, ndi zamoyo ndi akulu; ndipo mawerengedwe ao anali zikwi khumi kucurukitsa zikwi khumi ndi zikwiza zikwi;