1 Ndipo pamene anamasula cizindikilo cacisanu ndi ciwiri, munali cete m'Mwamba monga mwa nthawi ya ora latheka.
2 Ndipo ndinaona angelo asanu ndi awiri amene amaimirira pamaso pa Mulungu; ndipo anawapatsa malipenga asanu ndi awiri.
3 Ndipo anadza mngelo wina, naima pa guwa la nsembe, nakhala naco cotengera ca zofukiza cagolidi; ndipo anampatsa zofukiza zambiri, kuti aziike pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima onse pa guwa la nsembe lagolidi, lokhala ku mpando wacifumu.
4 Ndipo utsi wa zofukiza, pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima unakwera kuturuka m'dzanja la mngelo, pamaso pa Mulungu.
5 Ndipo mngeloyo anatenga mbale ya zofukiza, naidzaza ndi mota wopara pa guwa la nsembe, nauponya pa dziko lapansi; ndipo panakhala mabingu, ndi mau, ndi mphezi, ndi cibvomezi.
6 Ndipo angelo asanu ndi awiri akukhala nao malipenga anadzikonzera kuti aombe.
7 Ndipo woyamba anaomba, ndipo panakhala matalala ndi moto, zosanganiza ndi mwazi, ndipo anazitaya pa dziko lapansi; ndipo limodzi la magawo atatu a dziko lidapserera, ndipo limodzi la magawo atatu a mitengo lidapserera, ndipo msipu wonse udapserera.