4 Ndipo utsi wa zofukiza, pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima unakwera kuturuka m'dzanja la mngelo, pamaso pa Mulungu.
5 Ndipo mngeloyo anatenga mbale ya zofukiza, naidzaza ndi mota wopara pa guwa la nsembe, nauponya pa dziko lapansi; ndipo panakhala mabingu, ndi mau, ndi mphezi, ndi cibvomezi.
6 Ndipo angelo asanu ndi awiri akukhala nao malipenga anadzikonzera kuti aombe.
7 Ndipo woyamba anaomba, ndipo panakhala matalala ndi moto, zosanganiza ndi mwazi, ndipo anazitaya pa dziko lapansi; ndipo limodzi la magawo atatu a dziko lidapserera, ndipo limodzi la magawo atatu a mitengo lidapserera, ndipo msipu wonse udapserera.
8 Ndipo mngelo waciwiri anaomba, ndipo monga ngati phiri lalikuru lakupserera ndi mota Iinaponyedwa m'nyanja; ndipo limodzi la magawo atatu a nyanja linasanduka mwazi;
9 ndipo lidafa limodzi la magawo atatu a zolengedwa ziri m'nyanja, zokhala ndi moyo; ndipo limodzi la magawo atatu a zombo lidaonongeka.
10 Ndipo anaomba mngelo wacitatu, ndipo idagwa kucokera kumwamba nyenyezi yaikuru, yoyaka ngati muuni, ndipo idagwa pa limodzi la magawo atatu a mitsinje, ndi pa akasupe amadzi;