1 Ndipo pamene analikuturuka Iye m'Kacisi, mmodzi wa ophunzira ace ananena kwa Iye, Mphunzitsi, onani, miyala yotere ndi nyumba yotere.
2 Ndipo Yesu anati kwa iye, Kodi waona nyumba izi zazikuru? Sudzasiyidwa pano mwala umodzi pamwamba pa unzace, umene sudzagwetsedwa.
3 Ndipo pamene anakhala Iye pa phiri la Azitona, popenyana ndi Kacisi, anamfunsa Iye m'tseri Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Andreya, kuti,
4 Tiuzeni, zinthu izi zidzacitika liti? Ndi cotani cizindikilo cace cakuti ziri pafupi pa kumarizidwa zinthu izi zonse?
5 Ndipo Yesu anayamba kunena nao, Yang'anirani kuti munthu asakusoceretseni.
6 Ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Iye; nadzasoceretsa ambiri.
7 Ndipo m'mene mudzamva za nkhondo ndi mbiri zace za nkhondo, musamadera nkhawa: ziyenerakucitika izi; koma sicinafike cimariziro.