29 Ndipo Iye anati kwa iwo, Mtundu uwu sukhoza kuturuka ndi kanthu kena konse, koma ndi kupemphera.
30 Ndipo anacoka iwo kumeneko, napyola pakati pa Galileya; ndipo Iye sanafuna kuti munthu adziwe.
31 Pakuti anaphunzitsa ophunzira ace, nanena nao, kuti, Mwana wa munthu aperekedwa m'manja a anthu, ndipo adzamupha Iye; ndipo ataphedwa, adzauka pofika masiku atatu.
32 Koma iwo sanazindikira mauwo, naopa kumfunsa.
33 Ndipo iwo anadza ku Kapernao; ndipo pamene anakhala m'nyumba, Iye anawafunsa, Munalikutsutsana ninji panjira?
34 Koma iwo anakhala cete; pakuti anatsutsana wina ndi mnzace panjira, kuti, wamkuru ndani?
35 Ndipo m'mene anakhala pansi anaitana khumi ndi awiriwo; nanena nao, Ngati munthu afuna kukhala woyamba, akhale wakuthungo wa onse, ndi mtumiki wa onse.