1 PACIYAMBI panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau ndiye Mulungu.
2 Awa anali paciyambi kwa Mulungu,
3 Zonse: zinalengedwa ndi iye; ndipo kopanda iye sikunalengedwa kanthu kali konse kolengedwa,
4 Mwa iye munali moyo; ndi moyowu unali kuunika kwa anthu.