28 Zinthu izi zinacitika m'Betaniya tsidya lija la Y ordano, pomwe analikubatiza Yohane.
29 M'mawa mwace anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, 4 Onani Mwanawankhosa wa Mulungu 5 amene acotsa cimo lace la dziko lapasi!
30 6 Ndiye amene ndinati za iye, Pambuyo panga palinkudza munthu amene analipo ndisanabadwe ine; pakuti anali woyamba wa ine.
31 Ndipo sindinamdziwa iye; koma kuti aonetsedwe kwa Israyeli, 7 cifukwa ca ici ndinadzaine kudzabatiza ndi madzi.
32 Ndipo Yohane anacita umboni, nati, 8 Ndinaona Mzimu alikutsika kucokera Kumwamba monga nkhunda; nakhalabe pa iye.
33 Ndipo sindinamdziwa iye, koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzaona Mzimu atsikira, nakhala pa iye, 9 yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera.
34 Ndipo ndaona ine, ndipo ndacita umboni kuti Mwana wa Mulungu ndi Yemweyu.