31 Ndipo sindinamdziwa iye; koma kuti aonetsedwe kwa Israyeli, 7 cifukwa ca ici ndinadzaine kudzabatiza ndi madzi.
32 Ndipo Yohane anacita umboni, nati, 8 Ndinaona Mzimu alikutsika kucokera Kumwamba monga nkhunda; nakhalabe pa iye.
33 Ndipo sindinamdziwa iye, koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzaona Mzimu atsikira, nakhala pa iye, 9 yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera.
34 Ndipo ndaona ine, ndipo ndacita umboni kuti Mwana wa Mulungu ndi Yemweyu.
35 M'mawa mwacenso analikuimirira Yohane ndi awiri a akuphunzira ace;
36 ndipo poyang'ana Yesu alikuyenda, anati, 10 Onani Mwanawankhosa wa Mulungu!
37 Ndipo akuphunzira awiriwo anamva iye alinkulankhula, natsata Yesu.