4 Mwa iye munali moyo; ndi moyowu unali kuunika kwa anthu.
5 Ndipo kuunikaku kunawala mumdima; ndi mdimawu sunakuzindikira.
6 Kunali munthu, wotumidwa ndi Mulungu, dzina lace ndiye Yohane.
7 Iyeyu anadza mwa umboni kudzacita umboni za kuunikaku, kuti onse akakhulupirire mwa iye,
8 iye sindiye kuunikaku, koma anatumidwa kukacita umboni wa kuunikaku.
9 Uku ndiko kuunika kweni kweni, kumene kuunikira anthu onse akulowa m'dziko lapansi.
10 Anali m'dziko lapansi, ndi dziko linalengedwa ndi iye, koma dziko silinamzindikira iye.